MZUZU DIOCESE MOCK
2023 MALAWI SCHOOL CERTIFICATE OF EDUCATION EXAMINATION
CHICHEWA
Friday, March 24
Subject Number:M032/II
Time Allowed: 2hours
1:30-3:30pm
PAPER II
(Malikisi 90)
Malangizo
1. Onetsetsani kuti pepala lili ndi Funso Chongani Muno
funso ngati osalembamo
masamba osindikizidwa khumi ndi
mwayankha
awiri.
1
2. M’gawo A: Malamulo a chiyankhulo:
Yankhani mafunso onse. (Malikisi 40) 2
3. M’gawo B: Kumvetsa nkhani:
Yankhani mafunso onse: (Malikisi 20) 3
4. M’gawo C: Chifupikitso: (Malikisi 15)
4
5. M’gawo D: Chimasuliro. (Malikisi 15)
6. Lembani dzina lanu pamwamba pa
5
tsamba lililonse loyankhirapo.
7. Perekani pepalali kwa oyang’anira 6
mayeso nthawi ikakwana.
7
Total
Page 1 of 12
GAWO A (MALIKISI 40)
Malamulo a Chiyankhulo
• Langizo: Yankhani mafunso onse.
(i) a. Sinthani mneni ‘menya’ kuti akhale m’misintho ya aneni yotsatirayi.
(i) Womchitira ___________________________________(Malikisi 1)
(ii) wochititsitsa __________________________________ (Malikisi 1)
(iii) Wochitirana __________________________________ (Malikisi 1)
(iv) Wochititsa ___________________________________ (Malikisi 1)
b. Fotokozani momwe mayina ali munsimu adapangidwira
i. Mphunzitsi
________________________________________________________________

(Malikisi 2)
ii. Mwanapiye

iii. Likulu

2. a. Tsekani mzere kunsi kwa mimvekero ndipo mutchule magulu awo.
i. Agogo angoti khalu pampando.
_________________________________________________(Malikisi 2)
Page 2 of 12
ii. Sindingamwe madzi akuda bi.
_________________________________________________(Malikisi 2)
iii. Adangoti sokoloku kuchokera patchire.
_________________________________________________(Malikisi 2)
b. Perekani mitundu ya agwirizanitsi omwe ali ndi mzere kunsi kwawo
m’ziganizo zotsatirazi.
(i) Njiwa ziwiri zaoloka Nyanja.
______________________________________________________(Malikisi 1)
(ii) Benito wapeza zomwe amafuna.
______________________________________________________(Malikisi 1)
(iii) Mwana uyu wakhuta kwambiri.
______________________________________________________(Malikisi 1)
(iv) Amayi andipatsa ndalama.
______________________________________________________(Malikisi 1)
3. a. Lembani mitundu ndi ntchito za akapandamneni omwe ali ndi mzere
kunsi kwawo mziganizo zotsatirazi:
(i) Atsibweni ako sandifuna kwanu. (Malikisi 2)
Mtundu:__________________________________________________
Ntchito: __________________________________________________
(ii) Ndakhala ndikuphunzira kwa zaka zinayi. (Malikisi 2)
Mtundu: _________________________________________________
Ntchito: __________________________________________________
(iii) Amayo ine! M’mimba mwanga mukundipweteka. (Malikisi 2)
Mtundu: _________________________________________________
Ntchito: _________________________________________________
Page 3 of 12
b. Lembani ziganizo zomveka bwino ndi ‘li’ kusonyeza ntchito
zotsatirazi ndipo mutseke mzere kunsi kwake.
(i) Kukhala tsinde lamneni (Malikisi 2)
________________________________________________________________
(ii) Kukhala mphatikiramtsogolo woloza. (Malikisi 2)
________________________________________________________________
4. Phwanyani chiganizo chotsatirachi pounika mawu paokhapaokha.
Mwana wagwa chagada (Malikisi 10)

Page 4 of 12
GAWO B (Malikisi 20)
Kumvetsa Nkhani Ndi Kusanthula Chiyankhulo
5. Werengani nkhani ili m’munsiyi mosamala ndipo muyankhe mafunso
otsatirawo.
Udali usiku wa tsiku lina, pamene m’mudzi mwa Bokosi m’boma la Phalombe
mudadza chisokonezo chosaiwalika. Udali usiku wabwino ndithu anthu
akumverera kukoma kwa magombeza awo chifukwa cha mvula yomwe
idamanga nthenje m’derali kwa masiku angapo. Patsikuli anthu ambiri adagona
ndi makekhutu yemwe pamene kudamveka mkokomo wamphamvu wa madzi
amene amachokera m’phiri lotchedwa Michesi. Madziwa adaononga miyoyo ya
anthu ambiri, mbewu ngakhalenso ziweto ndi katundu osiyanasiyana. Patsikulo
kudalibe kuyang’ana m’mbuyo kwa amene anapeza mpata wothawa popeza
aliyense amafuna kupulumutsa moyo wake.
Anthu ambiri adayetsetsa kuthawira pasukulu yoyandikana nawo ya sekondale
ya Phalombe kuti adzipulumutse. Ngakhale kuti ku sekondaleko madziwo
sadafike m’nyumba zogonamo ndi zophunziramo, madziwa adasefukira ndi
kudzadza pa bwalo la masewera ampira wa miyendo lomwe lidamangidwa
m’munsi mwa zipilala zomwe anthu amakhalamo poonerera masewera. Anthu
ena omwe adatha kuthawa m’mudzi muja usikuwo, adakokoloka ndi kufa ndi
madzi omwe adadzadza pabwaloli pofuna kuti akafike ku nyumba zogonamo
ophunzirazo. Maliro adali dothi m’derali ngakhalenso ku sekondale ya
Phalombe makamaka mu holo popeza anthu omwe amathandiza kupulumutsa
anzawo adalinso kutola matupi a anthu ambiri omwe adafa pangoziyo ndi
kukawaika mu holoyo.
Mnyamata wina dzina lake Winesi Songola poona mitembo ya anthu omwe
adali kugwira ntchito za boma m’derali adachita chifundo ndi kutenga zovala
zake zonse komaso zofunda zake zonse ndi kuphimbira mitemboyo. Atafika a
Page 5 of 12
Bungwe la Malawi Red Cross motsogozedwa ndi nduna ya boma yoona za
ngozi zodza mwadzidzidzi a Lucius Chikuni panthawiyo, ndi kuona zimene
anachita mnyamatayo adamuuza kuti akadzamaliza maphunziro ake a sekondale
boma lidzamulemba ntchito ndipo adalembedwadi ntchito ndi bungwe la
Malawi Red Cross.
Pongokambapo pang’ono chomwe chidatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke
mnyanga pankhani ya kusefukira kwa madzi m’derali, chidali chakuti anthu
ozungulira m’midzi yomwe idali pafupi ndi phiri la Michesi adapeza mgodi
wawo m’phirimu posadziwa kuti akuika miyoyo yawo pachiswe. Adali ndi
chizolowezi chomaba mitengo pochita nkhuni, kuotcha makala ndi kupala
matabwa a malonda. Ngakhale kuti boma lidatumiza mlonda woteteza phirili,
anthuwa ankaba mitengo m’phirimo ndi usiku omwe. Boma lidayetsetsa
kuteteza phirili koma sizidaphule kanthu chifukwa cha uzayakunkhongo wa
anthu a m’derali. Zotsatira za mchitidwewu phiri lonse la Michesi lidasanduka
padazi. Padalibe chamoyo chomwe chikadapulumuka ku nkhanza za anthuwa.
Izi zidachititsa kuti chitetezo cha phirili chichepe kotero kuti m’phirimu
munabwera madzi omwe anakokolola ndi kuononga zinthu zambiri.
Panthawiyi boma lidayetsetsa kupeza njira zopulumutsira anthu; kotero kuti
lidatumiza ndege yomwe inabwera ndi kumatola anthu ena omwe adali
atakwera m’mitengo podzipulumutsa, nkumakawasiya ku sukulu ya sekondale
ya Phalombe. Zakudya zomwe anthuwa amadya zimatsitsidwa pandege
yomweyo kuchokera ku nyumba zosungiramo zakudya za Admarc.
Ngakhale kuti kudali chipatala chapafupi cha “Banja Loyera”, kudali kovuta
kuti wina akadwala akalandire thandizo la mankhwala popeza nawo mtsinje wa
Phalombe udali utafafanizika ndi madzi motero ndegezi zimanyamulanso anthu
odwala kupita nawo ku chipatala cha Zomba. Anthu a m’derali adauzidwa kuti
akhale zaka zisanu asakulima m’minda yawo popeza mitembo ya anthu akufa
idali kupezeka paliponse choncho kunali kofunika kuti mitemboyo iwole kaye.
Page 6 of 12
Izi zinachititsa kuti ana ambiri anyentchere ndi kumwalira chifukwa anthuwa
amadya mogenda.
Amayi ambiri ndi atsikana okhwima adasanduka afisi ndi cholinga chofuna
kupeza chakudya. Kudali kovuta ana kuti apite kusukulu za pulaimale kwa
miyezi itatu podikira kuti madzi aume. Izi zidasokoneza maphunziro a
ophunzirawo popeza sadalembe nawo mayeso otsiriza a chaka chimenecho
motero kuti adabwereza makalasi awo chaka chotsatiracho. Adauzidwanso kuti
asamange nyumba zawo pafupi ndi mtsinje komanso momwe munadutsa
madziwo popeza kuti mphechepeche mwa njovu sadutsamo kawiri. Anthuwa
adasamukira kumidzi yoyandikana nayo ndipo mpaka lero ndi kumene
akukhala. Anthu otsala am’mudzi mwa Bokosi adanong’oneza bondo
polingalira za unkhutukumve wawo ndipo adaphunzira katalumwa.
Tsopano yankhani mafunso otsatirawa m’ziganizo zomveka bwino.
(a).(i). Tchulani dzina la mudzi omwe udakhudzidwa ndi ngozi ya madzi
osefefukira.
________________________________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) Ndi ntchito ziwiri ziti zomwe zidayambitsa mchitidwe wodula mitengo
mopanda chilolezo m’phiri la Michesi? (Malikisi 2)
1. _________________________________________________________
2. _________________________________________________________
(iii) Perekani njira ziwiri zokha zomwe boma lidatsata pothandizira anthu
omwe adakhuzidwa ndi madzi osefukira mderali. (Malikisi 2)
1. _______________________________________________________
2. ________________________________________________________
Page 7 of 12
(iv) Tsimikizani kuti kusefukira kwa madzi m’mudziwu kudabweretsa
mavuto aakulu pa miyoyo ya anthu m’derali popereka mfundo ziwiri
zokha. (Malikisi 2)
1. _________________________________________________________
2. _________________________________________________________
(v) N’chifukwa ninji Winesi Songola adalembedwa ntchito ndi bungwe la
Red Cross? (Malikisi 2
_____________________________________________________________
____________________________________________________________
(vi) Tsimikizani kuti anthu a m’mudzi womwe udasefukira madziwu adali
osamva. (Malikisi 2)
_____________________________________________________________
_____________________________________________________________
b. Kusanthula chiyankhulo
i. Perekani matanthauzo a nsinjiro za chiyankhulo zotsatirazi zomwe
zikupezeka mu nkhani mwawerengayi.
1. maliro adali dothi
_________________________________________________(Maikisi 2)
2. lidasanduka padazi
________________________________________________ (Malikisi 2)
3. idamanga nthenje
_______________________________________________ (Malikisi 2)
ii. Pezani mawu mu nkhaniyi omwe akutanthauza izi:
1. adali mtulo ____________________________________ (Malikisi 1)
2. chomwe chidayambitsa
_____________________________________________ (Malikisi 1)
3. adadziwa atapeza mavuto
_____________________________________________________ (Malikisi 1)
Page 8 of 12
GAWO C: (MALIKISI 15)
CHIFUPIKITSO
6. Werengani nkhani yotsatirayi mosamala. Ili ndi mawu 122 ndipo
muifupikitse kuti ikhale ndi mawu osachepera 50 koma asapitirire 60.
GANIZA, MNYAMATA WOSASAMALA ASANDULIKA
Ganiza adali mnyamata yemwe amakhala mu mzinda wa Utale. Pakhomo pa
mnyamatayu padali posasiririka chifukwa chosowa ukhondo. Chifukwa cha
ichi matenda samamuchoka mnyamatayu ndipo iye amaganiza kuti wina wake
ndi yemwe amamuchita chipongwe popeza amagwira ntchito mu bungwe lina
mu mzindawu.
Tsiku lina mchimwene wake Samala adaganiza zokamuchezera mchimwene
wakeyu. Atafika pakhomo adasowa chonena poona uve womwe udali
pakhomopo. Adapeza kuti zovala za mchimwene wakeyu zimangopezeka
palipomse ngakhale ndi ku khitchini komwe. Mbale ndi mapoto zinali
zosatsuka ndipo zidangoti mbwee m’nyumba monsemo. Samala adasesa pa
bwalo ponse kuzungulira nyumbayo. Atatha apo, adatsuka bwino mbale ndi
mapoto ndikuzilongedza m’malo mwake. Adatoleranso zovala zomwe
zimapezeka paliponse m’nyumba ndi kuzilongedza m’malo mwake. Atatha
apo, adasesa ndikukolopa m’nyumba, kupuputa katundu yense woyenera
m’nyumbamo.
Pamene mkulu wake amaweruka ku ntchito madzulo adadzidzimuka atalowa
m’nyumbamo poyesa walowa m’nyumba yamwini. Amati azibwerera koma
ataona Samala adatsimikiza kuti sadasochere ayi.
Page 9 of 12

(Malikisi 15)
Page 10 of 12
GAWO D: (Malikisi 15)
CHIMASULIRO
7. Masulirani nkhani yotsatirayi m’Chichewa chomveka bwino..
Taking care of the natural resources
Natural resources are materials or substances such as forests, water, mountains
and soil that occur in nature that human beings should use. Of late, man has
become careless in the usage of these resources.
Many trees have been cut down carelessly. The cutting of trees has affected the
rainfall patterns. Instead of having long periods of rain, they are now short and
start late. As a result, some rivers are not getting enough water and often dry up.
If the trend of cutting down trees continues at this alarming rate, man will face
many problems.

Page 11 of 12

MAFUNSO ATHERA PANO
Page 12 of 12